...
MWAZIZIWA? > ZINA UKAMVA > ANTHU AKAKWIYA SAONASO KUTI UYU NDI NDI PRESIDENT WATHU, KAYA NDI BWANA

ANTHU AKAKWIYA SAONASO KUTI UYU NDI NDI PRESIDENT WATHU, KAYA NDI BWANA

MALAWI POLICE

Mwaimva? nkhani yomwe ili apa ndi yoopsa kwambiri imene ngakhale apolice sakumvesa kuti amalawi akakwiya angafike apa. Akutitu Apolisi m’boma la Ntchisi anjata anyamata 12 omwe amagwira ntchito ku kampani ya Malawi Electricity Access Project (MEAP) kaamba koti anamangilira akuluakulu awiri akampaniyi kumitengo pomwe amafuna kukakamiza akuluakulu akampaniyi kuti awapatse malipiro awo.

Mneneri wa polisi ya Ntchisi a Salome Zgambo atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati nkhaniyi itazindikilidwa pa 24 May inapatsa anthu mantha zomwe zinapangitsa kuti apolisi alowelerepo pankhaniyi ndi kumanga oganiziridwa khumi ndi awiriwa.

A Sitima ati oganiziridwawa ndi a Yobe Frackson,, a Andrew Banda, Moses Kaluba, Charles Chibwana, Emanuel Masanje, a Thomas Kambani, Godfrey Banda, Siko Kasambeni ndi a Desire Kachigodi.

Maligana ndi a Zgambo, oganiziridwawa ali mchitolokosi kuti akayankhe mulandu odzetsa chisokonezo pa malo antchito komanso kuphwanya ufulu wa anthu ena.


ENGLISH VERSION

Police in Ntchisi district have arrested 12 young men working for the Malawi Electricity Access Project (MEAP) for allegedly tying two company officials to trees while trying to force the company to pay them their salaries.


Ntchisi police spokesperson Salome Zgambo confirmed the incident and said that when the incident was reported on May 24, it created panic among the people, prompting the police to intervene and arrest the 12 suspects.


Sitima said the suspects are Yobe Frackson, Andrew Banda, Moses Kaluba, Charles Chibwana, Emanuel Masanje, Thomas Kambani, Godfrey Banda, Siko Kasambeni and Desire Kachigodi.
Along with Zgambo, the suspects are in custody awaiting trial on charges of causing disorder in the workplace and violating the rights of others.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Seraphinite AcceleratorOptimized by Seraphinite Accelerator
Turns on site high speed to be attractive for people and search engines.