...
MWAZIZIWA? > ZINA UKAMVA > KODI NDI ZA KUCHIPINDA ZOMWE UYU WAPHELA MKAZI WAKE?

KODI NDI ZA KUCHIPINDA ZOMWE UYU WAPHELA MKAZI WAKE?

MURDERED WIFE

Koma abale zina ukamva mmmh, Akuti Ku Chiradzulu apolisi amanga a Dyson Makawa powaganizila kuti apha mkazi wawo atasemphana pa nkhani zam’banja.

Mneneri wa polisi m’bomali, a Cosmas Kagulo awuza Zodiak Online lero kuti a Makawa akuganiziridwa kuti anapha mkazi wawo Zione John yemwe anasiyana nayo atasemphana maganizo.

Iwo ati pa 17 mwezi uno a Makawa anakumana ndi akazi awowa pa msika wa Makiliyere m’bomali pomwe anayamba kumenyana atakana kuti abwelelane.

Malemuwa anawatengela ku chipatala chachikulu cha Zomba atakomoka ndipo anamwalilira ku chipatalachi maka kamba ka ku vulala m’mutu.

Malemuwa amachokela m’mudzi mwa Kawawa pomwe a Dyson Makawa amachokera m’mudzi mwa Mauwa mfumu yaikulu Chitera M’bomali.


ENGLISH VERSION OF THIS

In Chiradzulu, police have arrested Dyson Makawa on suspicion of killing his wife after a domestic dispute.

Police spokesperson in the district, Cosmas Kagulo, told Zodiak Online today that Makawa is suspected of killing his wife Zione John, whom he separated from after a disagreement.

He said that on the 17th of this month, Makawa met his wife at the Makiliyere market in the district when they started fighting after she refused to leave.

The deceased was taken to Zomba General Hospital after collapsing and died at the hospital from head injuries.

The deceased hailed from Kawawa village while Dyson Makawa hailed from Mauwa village, a major chief in Chitera in the district.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Seraphinite AcceleratorOptimized by Seraphinite Accelerator
Turns on site high speed to be attractive for people and search engines.