NKHANI YOKUPHA MWANA NDI KUTHAWA
Mtsikana wachichepele dzina lake Ava Moore, yemwe anali ndi zaka 18 zokha, anamwalira atagundidwa ndi jet ski pamene anali kosangalala m’nyanja. Izi zinachitika kumapeto kwa sabata m’nyanja imene ili ku Texas.
Mayi wina wazaka 21, dzina lake Daikerlyn Gonzalez, ndiye amene anali kuyendetsa jet ski. Uyu ndi wochokera ku Venezuela ndipo analowa m’dziko popanda zikalata zovomerezeka. Apolisi ananena kuti ankayendetsa jet ski mothamanga kwambiri pafupi ndi m’mphepete mwa nyanja ndipo anakumana ndi kayak ya Ava.
Ava anatengedwa kuchipatala, koma anamwalira kumeneko.
Gonzalez anali ndi mayi wina pa jet ski nthawi ya ngoziyo. Ataona kuti zagwa, onse awiri anathawa. Koma pambuyo pake, munthu amene anali naye pa jet ski anabwerera n’kukayankhula ndi apolisi. Gonzalez anathawa limodzi ndi chibwenzi chake, Maikel Perozo, mu galimoto. Ali m’njira yothawira, anakumana ndi ngozi ina pogundana ndi magalimoto awiri ena.
Apolisi anawamanga mu mzinda wotchedwa Dallas.
Tsopano Gonzalez akumangidwa chifukwa chachikulu chotchedwa manslaughter, kutanthauza kuti wapha munthu osati mochita kukonza kapena kuti kufuna kumupha. Iye akhoza kulandira chilango cha zaka ziwiri mpaka zokwana 20 m’ndende.
Chibwenzi chake, Perozo, nayenso akumangidwa pa mlandu wina wochepa chifukwa chothandiza Gonzalez kuthawa ndi kugundana ndi magalimoto ena. Mayi wina amene anali pa jet ski sanamangidwe.
Gonzalez ndi Perozo onse ndi ochokera ku Venezuela. Analowa m’dzikolo mosavomerezeka. Izi zapasa chidwi cha akuluakulu a za imigileshoni komanso aboma.
Mmodzi mwa akuluakulu ananena kuti, “Ava ayenera kuti akadakali ndi moyo lero ndikukonzekera kulowa m’gulu lankhondo la mlengalenga.” Ngakhale bwanamkubwa wa Texas ananena kuti Gonzalez akuyenera kulandira chilango cha imfa.
Apolisi a za imigretioni ananena kuti Gonzalez ndi Perozo abweleretsedwa kwawo atangomaliza mlandu wawo.
One thought on “NKHANI YOKUPHA MWANA NDI KUTHAWA”