...
MWAZIZIWA? > ZA BUSINESS > LA 40 LAKWANA – AMAPHA ANTHU USIKU AJA AWAGWIRA.

LA 40 LAKWANA – AMAPHA ANTHU USIKU AJA AWAGWIRA.

THUGS

Mwaziziwa? Zachitika lero ku Lilongwe, akuti Apolisi amanga anthu 108 omwe akuwaganizira kuti akhala akubera anthu komanso kupha, ku Kanengo ndi madera ena ozungulira.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ku Central West Region a Foster Benjamin wati anthuwa amangidwa mosiyanasiyana pa ntchito yomwe apolisi akhala akugwira masiku apitawa kutsatira ma lipoti a umbanda komanso kuphedwa kwa anthu ku Kanengo.

Anthuwa malinga ndi a Chigalu ndi a zaka za pakati pa 18 ndi 48 ndipo ena mwa iwo anapezeka ndi chamba, mowa osavomelezeka, mafuta a galimoto ndi zina.

Apolisi a ku Kanengo, Kawale, Lilongwe ndi Lingadzi ndi omwe akhala akugwira ntchito yofuna kuthetsa umbandawu pokhazikitsa chitetezo mmadera monga Mgona, Area 25, Area 49 Mvama komanso mtsinje wa Nankhaka.

Malipoti omwe akhala akumveka msabatayi akusonyeza kuti anthu asanu aphedwa m’derali ndipo ena avulazidwa ndi akuba omwe akumamenya ndikubera anthu madzulo.

Wolemba Cathy Maulidi ku Times

ENGLISH VERSION

Police in Lilongwe have arrested 108 people suspected of kidnapping and murder in Kanengo and surrounding areas.

Central West Region Deputy Police Spokesperson Foster Benjamin said the arrests were made in separate operations carried out by police in recent days following reports of kidnappings and murders in Kanengo.

The suspects, according to Chigalu, are between the ages of 18 and 48 and some of them were found in possession of marijuana, illegal alcohol, motor oil and other items.

Police in Kanengo, Kawale, Lilongwe and Lingadzi have been working to curb the crime by establishing security in areas such as Mgona, Area 25, Area 49 Mvama and the Nankhaka River.

Reports this week indicate that five people have been killed in the area and others injured by robbers who have been beating and robbing people in the evening.

Written by Cathy Maulidi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Seraphinite AcceleratorOptimized by Seraphinite Accelerator
Turns on site high speed to be attractive for people and search engines.