MUNTHU WABELA MCHIMWENE WAKE KOMA MPAKA KUMUTELE ABALE?
Kodi abale nkhani iyi mukuyimva bwanji? akuti bwalo la Milandu m’boma la Mangochi lalamula Mayi wina wazaka 31 kuti akakhale kundende zaka zitatu atapezeka olakwa pa Mulandu wakuba katundu wa mchimwene wake wandalama zokwana K12 million.
Oyimila Boma pa Mlanduwu Grace Mindozo anawuza bwalori kuti chaka chatha, mayi Cecelia Liotcha ankasunga katundu wa mchimwene wawo yemwe ali mdziko la South Africa.
Koma Sabata yathayi, m’modzi mwa achimwene a Mayiyu anazindikira kuti katundu wina monga Injini ya Galimoto, zitseko, Penti wa Nyumba, komanso Njinga zakapalasa zasowa mnyumbamo.
Ndipo nkhaniyi inatengeledwa ku polisi komwe kafukufuku wawo analoza chala mayiyu.
Mayiyu atamangidwa, analondolera a polisi kwa ena mwa anthu omwe anagula katunduyu.
Ndipo atawonekera ku bwalo la milandu, mayiyu anavomela mlanduwu koma anapempha bwalori kuti limuvele chisoni popeza ali ndi mwana wazaka ziwiri yemwe akuyamwitsa.
Koma bwalori linagamulabe kuti apite kundende kwa zaka ziwiri popeza kuti anawonetsa kusakhulupilika pogulitsa katundu wa mwini.
Mayi Cecilia Liotcha amachokela mmudzi mwa Mapira, Mfumu yayikulu Mapira, M’boma la Mangochi.