...
MWAZIZIWA? > ZA BUSINESS > PHONE YA IPHONE IKWELASO MTENGO OSAFUNA ASIYE

PHONE YA IPHONE IKWELASO MTENGO OSAFUNA ASIYE

Kodi inu amene mumafuna mutagula Iphone kapena muli nayo kale mukufuna mupange upgrade, Mwaimva iyi? Akuti anthu ogwiritsa ntchito lamya za IPhone atha kumazigula pa mtengo okwera ngati mtsogoleri wa dziko la America, a Donald Trump, apitilire ndi ganizo lake loyika msonkho wa 25 percent pa lamyazi zomwe imapanga ndi kampani ya Apple.

A Trump anena pa tsamba lawo la m’chezo la Truth Social, poopseza kampani ya Apple kuti isinthe ganizo lake lopangira lamyazi kunja kwa dziko la America.

Iwo ati akufuna kuti kampani ya Apple idzigulitsa mdziko la America ma IPhone omwe yapanga komweko osati kuchokera m’maiko ena.

Malipoti akuonetsa kuti kampani ya Apple ikufuna kusamutsa ntchito zake zopanga IPhone mdziko la China kupita ku India komanso Vietnam kutsatira misonkho yokwera yomwe Trump anaika pa katundu ochokera ku China kulowa ku America.

Mu nkhani ngati yomweyi, Trump waopsezanso kuti atha kuyika msonkho wa 50 percent pa katundu ochokera m’maiko omwe ali pansi pa European Union.

Did you know? iPhone users could be facing a steep price hike if US President Donald Trump goes ahead with his plan to impose a 25 percent tariff on Apple products.
Trump has threatened to change his stance on manufacturing iPhones outside the US, in a tweet on his Truth Social media account.
He said he wants Apple to sell iPhones made in the US instead of importing them from other countries.
Reports suggest that Apple is considering moving its iPhone manufacturing operations from China to India and Vietnam in response to Trump’s proposed tariffs on Chinese imports.
In a related development, Trump has also threatened to impose a 50 percent tariff on imports from the European Union.

One thought on “PHONE YA IPHONE IKWELASO MTENGO OSAFUNA ASIYE

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Seraphinite AcceleratorOptimized by Seraphinite Accelerator
Turns on site high speed to be attractive for people and search engines.