KOMA AWAWA ANGANENE IZI KUCHIPINDA KWA MCP CHAKWERA AKUMVA?
Mwaimva? Akutitu wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha Peoples PP, mchigawo chapakati, a Peter Kamange, auza anthu ku Mchinji kuti chipanichi motsogozedwa ndi mtsogoleri wake a Joyce Banda ndiwokonzeka kuthetsa mavuto azachuma omwe ali mdziko muno pano miyezi isanu ndi umodzi yokha atangotenga boma.
A Kamange , anena izi pamsonkhano omwe anachititsa pa bwalo la Magawa.
Iwo anati mu zaka ziwiri zomwe a Banda analamulira dziko lino anakwanitsa kuphula dziko lino pa mavuto monga kusowa kwa mafuta agalimoto, ndalama zakunja komanso kuthana ndi mavuto a maubale omwe dziko lino limakuna nawo.
Pamsonkhanowu, a Kamange anatinso chipanichi chikukambirana ndi zipani zina pofuna kupanga mgwirizano koma zambiri a Malawi adziwa zonse zikakonzeka.
ENGLISH VERSION
The Peoples Party (PP) deputy leader in the Central Region, Peter Kamange. Has told people in Mchinji that the party, led by its leader Joyce Banda, is ready to solve the country’s economic problems just six months after taking power.
Mr Kamange said this at a meeting he held at Magawa Stadium. He said that in the two years that Banda ruled the country, he managed to overcome many problems. Problems such as fuel shortages, foreign exchange and resolving the problems of relations that the country is facing.
At the meeting, Mr Kamange also said that the party is in talks with other parties. Talks to form a coalition but most Malawians will know when everything is ready.