ANTHU ANDEVU ZAWO KUMAPANGA IZI ZOONA?
Nde mwaimva ya lero? akutitu apolisi ku Salima amanga abambo atatu kaamba kopezeka ndi migolo khumi ndi inayi ya mafuta a petulo okwana malita 200 uliwonse.
Woyankhulira polisi ya m’bomali a Rabecca Ndiwate atsimikiza za izi ponena kuti anthu atatuwa ndi a Fatsan Phiri,Madalitso Dzindiwo komanso a Amidu Sipolo ndipo agwidwa loweluka ku Sengabay apolisi atatsinidwa nkhutu ndi anthu akufuna kwabwino.
Mafuta obedwa ndi amenewo….
Iwo ati oganizilidwawa anavomela za katunduyu ndipo atafunsidwa zamapepala owayenereza kukhala ndikatunduyu anakanika kutero zomwe zinapangitsa kuti apolisiwa awamange.
Anthu onsewa amachokera mdera la mfumu yayikulu Maganga mmudzi wa Dalankwanda m’mboma lomweli ndipo akuyembekezeka kukawonekera kubwalo la milandu posachedwa kuti akayankhepo pa mlandu wawo.
NTCHITO ILIPO
ENGLISH VERSION…..
Police in Salima have arrested three men for allegedly possessing fourteen 200-litre barrels of petrol.
Police spokesperson Rabecca Ndiwate confirmed the arrest, saying the three men were identified as Fatsan Phiri, Madalitso Dzindiwo and Amidu Sipolo and were arrested in Sengabay on Sunday after police were ambushed by well-wishers.
They said the suspects confessed to the crime and when asked for the documents required to possess the goods, they failed to do so, prompting the police to arrest them.
All the suspects hail from the Maganga chiefdom in Dalankwanda village in the same state and are expected to appear in court soon to answer their charges.