KALINDO WAFIKA KALE KU MZUZU KOPANGA MA DEMO – APA ZAYIPA BASI
Mwaimva? akutitu yemwe ndi mtsogoleri wa gulu la Malawi First a Bon Kalindo wafika pabwalo lamasewelo la Katoto pomwe akhale akuchita nawo ziwonetselo zomwe zakonzedwa.
A Kalindo ati iwo ndi m’malawi ndipo ziwonetselozi akupangitsanso ndi a Malawi ndichifukwa chake aganiza zopanga nawo ziwonetselozi Ku Mzuzu.
Iwo ati siokondwa ndi kukwela Kwa mitengo ya zinthu komanso kuti nthambi ya MEC igwilise ntchito ndondomeko ya smartmaric pa chisankho.
A Kalindo atinso ziwonetselozi ndizabata popeza iwo akungofuna kutumiza uthenga kuboma zamavuto omwe alipo mdziko muno.
Ndipo a Lyton Mangochi wati chisankho sichitika pokha pokha ngati ndondomeko yomwe angagwilitse ntchito ndiyakale.
ENGLISH VERSION OF THIS
The leader of the Malawi First party, Bon Kalindo, has arrived at the Katoto Stadium where he will be participating in the planned demonstrations.
Mr. Kalindo said that he is from Malawi and that these demonstrations are also being organized by Malawians, which is why he decided to join the demonstrations in Mzuzu.
He said that he is not happy with the increase in prices of goods and that the MEC branch is using the smartmaric system in the elections.
Mr. Kalindo also said that the demonstrations are peaceful because they only want to send a message to the government about the problems that exist in the country.
And Mr. Lyton Mangochi said that the elections will not be held unless the system they use is outdated.