...
MWAZIZIWA? > ZINA UKAMVA > KODI IYISO NDE KAMPENI YANJI YOMWE SYMON KENDAL WAPANGAYI?

KODI IYISO NDE KAMPENI YANJI YOMWE SYMON KENDAL WAPANGAYI?

Oyimba wodziwika bwino m’dziko lino a Kendall Kamwendo yemwenso akufuna kudzapikisana nawo pa chisankho cha 16 September pa mpando wa phungu wa dera la Dowa Mndolera ngati phungu woyima payekha m’boma la Dowa lero wapereka Ambulance yoti izithandiza kutumikira anthu pa ntchito za umoyo kudelari.

A Kamwendo ati agula ambulance yi ndi ndalama zawo kaamba koti iwo akudziwa mavuto amene anthu akuderali akukumana nawo pankhani za umoyo komanso zitukuko zosiyanasiyana monga madzi aukhondo milatho,mwayi wa ngongole za NEEF, nyumba zophuziliramo komanso nyumba za aphuzitsi ndi zina zambiri.

SYMON AND KENDAL MP

“Nthawi yakwana yoti anthu kudera la Mndolera alandire zitukuko zimene akhala akuzisowa kwa nthawi yayitali ndipo ndikukuwuzani kuti ine ndidzapereka zitukukuko mosakondera dera komanso ndidzaonetsetsa kuti ndalama za Constituency Development Fund CDF zikugwira ntchito yosintha miyoyo ya athu m’dera lino,” anatero a Kamwendo.

Iwo pempha anthu kudelari kuti adzawavotere pa chisankho chimene chikubwerachi kaamba koti iwo ndi mwana wa kudelari komanso ali ndi masomphenya otukula delari.

Iwo awapempha anthuwa izi lero pamene amaonetsa ambulance kwa anthu akuderali komanso kuyipereka kwa mfumu yayikulu Kayembe ndi Dzoole.

Mfumu yayikulu Kayembe ya m’derali yayamikira zomwe achita a Kamwendo ati kaamba koti anthu akuderali amayenda Mitundu italiitali ndi matenda panjinga komanso pangolo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Seraphinite AcceleratorOptimized by Seraphinite Accelerator
Turns on site high speed to be attractive for people and search engines.