...
MWAZIZIWA? > ZINA UKAMVA > KOMA ABALE MUNTHU KUMUTELE ZOONA?

KOMA ABALE MUNTHU KUMUTELE ZOONA?

Kodi apapa nde tinene kuti kwayambika zotani nanga? Akuti apolisi m’boma la Mulanje akusakasaka anthu omwe apha ndikuotcha a Luka Saluwa a zaka 35 kaamba koti amawaganizira kuti anapha mayi Rita Maluku a zaka 43 ochokera kwa Misomali Kwa mfumu yaikulu Chikumbu m’boma la Mulanje.

M’neneri wapolisi ya m’bomali a Innocent Moses ati lachitatu sabata ino mayi Maluku anapita ku mtsinje kukachapa komwe sanabwere zomwe zinachititsa kuti abale ndi anthu amudzi ayambe kuwasakasaka.

A Moses ati ali mkati mosakasaka thupi lamayiwa linapezeka kwa oganizilidwawa ataliduladula ndikuliwamba.

“Kudzera mukafufuku wathu tapeza kuti aSuliwa omwe anapha mayiyu anali ndi mavuto amalingaliro angwiro ndipo m’chaka cha 2024 anagonekedwa ku chipatala cha Zomba Mental “, Moses anafotokoza.

Ndipo zosatira zachipatala zikusonyeza kuti a Suliwa amwalira kaamba kotaya magazi.

A Suliwa amachokera Mudzi wa Mabi mfumu yaikulu Chikumbu.

SOURCE : TIMES 360 MALAWI.

Police in Mulanje district are searching for the people who killed and burned Luka Saluwa, 35, on suspicion of killing Rita Maluku, 43, from Misomali Kwa, the chief of the Chikumbu clan in Mulanje district.
Police spokesperson Innocent Moses said on Wednesday that Ms Maluku went to the river to wash her body but did not return, prompting relatives and villagers to search for her.
Mr Moses said that during the search, the body of the deceased was found by the suspects, who had cut it into pieces and dismembered it.
“Through our investigation, we have found that Mr Saluwa, who killed the woman, had serious mental problems and was admitted to the Zomba Mental Hospital in 2024,” Moses explained.
Medical records indicate that Mr Saluwa died of blood loss.
Mr Saluwa is from the village of Mabi, the chief of the Chikumbu clan.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Seraphinite AcceleratorOptimized by Seraphinite Accelerator
Turns on site high speed to be attractive for people and search engines.