...
MWAZIZIWA? > ZINA UKAMVA > KUGULISA MWANA NGATI MBUZI PA MTENGO WA K2,000,000

KUGULISA MWANA NGATI MBUZI PA MTENGO WA K2,000,000

Eeeh koma KUTI mumve inuyo izi mmmh! Zimene zachitika ku South Africa zili ngati nthano komanso maloto.

Akuti Mayi wina dzina lake Racquel “Kelly” Smith wachita zachilendo kwambiri, mpaka ma Judge owelura sanakhulupirire izi atamva. Mai uyu anagulitsa mwana wake wa zaka 6, dzina lake Joshlin, ngati akugulitsa nsima pamsika! Ndipo kuyimvetsetsa bwino nkhaniyi, akuti anagulitsa mwana wake pa $1,100, imene ili ngati K2,000,000 ku Malawi kuno — zili ngati kugulitsa mwana ngati akugula firiji yogwiritsidwa ntchito kale kapena akugulisa njinga!

Koma pa khothi panalibe kumusekelera mai uyu. Mpaka judge anati, “Palibe chifukwa chilichonse chondichititsa kukupatsa chilango chochepa mai oyipa iwe.” Choncho, amumanga moyo wake wonse chifukwa chogulitsa munthu, komanso zaka 10 zowonjezera chifukwa chobera mwana — ngati kuti moyo wake onse ku ndende zachepa kapena sizinali zokwanira!

Komatu si yekha amene anali pa mlanduwu. Chibwenzi chake, Jacquen Appollis, komanso mnzake, Steveno van Rhyn, nao anawamanga moyo wonse. Ndi ngati anayambitsa “gulu la anthu opanda umunthu komanso gulu la zigawenga” mwina akuganiza kuti ndende ndi malo a holiday.

Koma nanga Mwana uyu Joshlin, zinamuthela bwanji?

Iye anangosowa mu February 2024, mu dela lotchedwa Middelpos ku Western Cape. Mpaka lero, sanapezekebe. Apolisi akulimbikira kufufuza usana ndi usiku. Mkulu wa apolisi ku Jon ko wati, “Sitigona mpaka titadziwa chimene chinachitika kwa mwanayu.”

KOMA SONO MA UMBONI ANATI BWANJI?.

Anthu amene anapereka umboni ku khothi anati Kelly anagulitsa mwana wake kwa Sangoma — uyu nde msing’anga wanini wa wamankhwala achikuda — amene anati akufuna mwanayo chifukwa cha maso ake ndi khungu lake. Munthu oyipa, kumafuna zikopa za munthu ngati kuti ndi mbuzi?

Mnzake woyandikana naye ananena kuti Kelly anamuuza mwachindunji kuti anagulitsa mwanayo. Ndipo m’busa wina ku mu dela lo anati, Kelly anali kale ndi mapulani a “Gula M’modzi, Pezani Wina Mwaulere” ija amati (Buy 1 get another for free ngati pizza ija) pa ana ake ena mu 2023akuwapereka pa $275 aliyense! Tangoganizani zimenezo! Ana mpaka ma discount! Moyo wa munthu zoona?

Mudzi wonse waopsezedwa. Oweruza wati mudzi wa Middelpos wasweka mtima, ndipo anthu akuvutika kukhulupirira.

Phunziro la nkhaniyi? Musagulitse ana anu. Osati chifukwa cha ndalama. Osati chifukwa cha mbuzi. Osatinso chifukwa cha Wi-Fi yaulere!

One thought on “KUGULISA MWANA NGATI MBUZI PA MTENGO WA K2,000,000

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Seraphinite AcceleratorOptimized by Seraphinite Accelerator
Turns on site high speed to be attractive for people and search engines.