...
MWAZIZIWA? > ZINA UKAMVA > KUTUKWANISA CHAKWERA OSALAKWA UKU ~ MBAVA ZA AZIMAYI AZIPANGA IZI KU LILONGWE KWA MCP

KUTUKWANISA CHAKWERA OSALAKWA UKU ~ MBAVA ZA AZIMAYI AZIPANGA IZI KU LILONGWE KWA MCP

MWAIMVA? Akutitu apolisi ku Lilongwe amanga amayi atatu omwe akuwaganizira kuti mothandizidwa ndi anthu ena anathyola mnyumba ndikubamo katundu monga deep freezer, upright fridge, mattress, microwave ndi katundu wina.

Amayiwa, malinga ndi mneneri wa polisi a Hastings Chigalu ndi a Chimwemwe Chembe a zaka 39, a Elizabeth Mkwezalamba a zaka 36 komanso a Memory Elias a zaka 46.

A Chigalu ati, woganiziridwa m’modzi (Chimwemwe) amakhala mnyumba yomwe mwini wake anapita ku Blantyre kukagwira ntchito zina ndipo mwini nyumbayo anatsekera katundu wina ofunika kuchipinda china mnyumbamo.

“Mayi Chimwemwe anauza mzawo Elizabeth kuti abe microwave inatsekeredwa kuchipindako mu njira yoonetsa kuti kunyumbako kunathyoledwa ndi okuba. Koma a Chimwemwe ngakhale anafikira a Elizabeth ndi nkhaniyi, anathyola chipindacho okha ndikubamo microwave-yo yomwe anakagulitsa K30,000,” atero a Chigalu.

Malinga ndi a Chigalu, a Elizabeth ataona kuti Chimwemwe wapindula yekha, anafikira mzawo Memory yemwe anagwirizana kuti akathyole kunyumbako ndikubamo katundu wina ofunikira ndipo kuti katunduyo akasungidwe kwa mayi Memory chifukwa a Elizabeth ankati mamuna wawo sangalore kusunga katundu okuba.

“Kenako mayi Memory anapeza anyamata atatu kuphatikizapo mwana wawo kuti akathandizire kubako ndipo anatengana kupita kunyumbako kuti anyamatawo akaone bwinobwino katundu ofunika kuti abedwe. Pa nthawiyo Chimwemwe sanali kunyumbako. Ndipo pa ulendo wawo wokaba usiku katunduyo anabedwa,” atero a Chigalu.

Pakadali pano apolisi akusaka anyamata atatu omwe anathandizira kubako. Komabe izi zisapangise kuti tiyiwale nkhani ya anyamata awiri awa amene ndi achimizi koma amakwera ndege kambirimbiri pa mwezi kodi amenewa amawapangila izi ndani? nkhani yawo yonse iyi, dinani button ili pasipa.


ENGLISH VERSION OF THIS


Police in Area 36 in Lilongwe have arrested three women on suspicion of stealing various household goods including two refrigerators, a mattress, a microwave; and hiring three other criminals to help them commit the theft.
According to Lilongwe police spokesperson Hastings Chigalu, the women are Chimwemwe Chembe, 39, Elizabeth Mkwezalamba, 36, and Memory Elias, 46. He said one of the suspects, Chimwemwe Chembe, lives in a house where the owner left to work in Blantyre, but he hid some of his belongings in one of the rooms.


The suspect, Chembe, allegedly told the second suspect, Elizabeth Mkwezalamba, about the items, informing her of the plan to steal a microwave from a locked room. He said that Chembe, however, stole the microwave and sold it for 30,000 kwacha.
But the second suspect, in turn, asked his friend, the third suspect, Memory Elias, to help him find people to break into the house where the goods were, and to help him hide the goods, as his husbands would not allow him to keep stolen goods.
Mr. Elias found three men, including his son. And, that night, the thieves he had hired broke into the house, stealing the goods. The police arrested the three women after they were caught, while all three men are still at large.

One thought on “KUTUKWANISA CHAKWERA OSALAKWA UKU ~ MBAVA ZA AZIMAYI AZIPANGA IZI KU LILONGWE KWA MCP

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Seraphinite AcceleratorOptimized by Seraphinite Accelerator
Turns on site high speed to be attractive for people and search engines.