...
MWAZIZIWA? > ENTERTAINMENT > MUKHALIRA CHI TOWN CHOMWECHO KOMA AWA ZAWO ZINAYELA

MUKHALIRA CHI TOWN CHOMWECHO KOMA AWA ZAWO ZINAYELA

Anyamata ambiri amazimva kuyimba kapena kumvela nyimbo za ma yoo. Koma nkhani ya lero ndi yodabwisa kwambiri. Tamveselani izi, akuti gulu loyimba la Madalitso Band momwe muli Yosefe Kalekeni ndi Yobu Maligwa, labowolanso mtambo kupita ku ulaya komwe akukaimba.

Gululi lomwe limapita chaka ndi chaka kukayimba kuyambira chaka cha 2017 pomwe adatenga chikoka ku phwando la Sauti za Busara ku Tanzania, ulendo uno akuyembekezeka kuponda ma dansi wosachepera makumi asanu.

Ulendo uno gululi likhala likuyimba ku United Kingdom, Germany, France, Norway komanso Switzerland ndipo likuyembekezeka kubwerera kumudzi kumapeto a mwezi wa August chaka chino.

Gululi lomwe ndilaku Ntandire mu mzinda wa Lilongwe,limayang’anilidwa ndi Neil Nayar yemwenso ndi woyimba ndi Emmanuel Kamwenje.

3 thoughts on “MUKHALIRA CHI TOWN CHOMWECHO KOMA AWA ZAWO ZINAYELA

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Seraphinite AcceleratorOptimized by Seraphinite Accelerator
Turns on site high speed to be attractive for people and search engines.